Masalimo 79:11 - Buku Lopatulika Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu; monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu; monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumve kubuula kwa anthu am'ndende, muŵasunge ndi mphamvu zanu zazikulu anthu oyenera kuphedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu; ndi mphamvu ya dzanja lanu muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe. |
Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, chipulumutso chathunso m'nthawi ya mavuto.
kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi.
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,