Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mivi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ake a Saulo, Abenjamini.
Masalimo 78:9 - Buku Lopatulika Ana a Efuremu okhala nazo zida, oponya nao mauta, anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana a Efuremu okhala nazo zida, oponya nao mauta, anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale Aefuremu anali ndi mauta, komabe adathaŵa pa tsiku la nkhondo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta, anathawabe pa nthawi ya nkhondo; |
Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mivi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ake a Saulo, Abenjamini.
koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda.
Ndi nkhondo ya Israele inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israele, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo.
Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji?
Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa.
Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi.