Koma sanamvere, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirire Yehova Mulungu wao.
Masalimo 78:8 - Buku Lopatulika Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikike ndi Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asakhale ngati makolo ao, anthu oukira ndi osamvera aja, mbadwo wa anthu amene mitima yao inali yosakhazikika, amene moyo wao unali wosakhulupirika kwa Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo asadzakhale monga makolo awo, mʼbado wosamvera ndi wowukira, umene mitima yake inali yosamvera Mulungu, umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye. |
Koma sanamvere, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirire Yehova Mulungu wao.
Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.
Komatu misanje siinachotsedwe; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.
wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.
Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene analakwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya.
Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.
Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.
kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israele, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe chomwe ndikuchitireni.
Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.
Ndipo ndinati kwa ana ao m'chipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;
Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.
ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;
Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.
Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine!
Yehova ananenanso ndi ine, ndi kuti, Ndapenya anthu awa, taona, awa ndi anthu opulukira;
M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,
Monga ntchito zao zonse anazichita kuyambira tsiku lija ndinawatulutsa ku Ejipito, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu ina, momwemo alikutero ndi iwenso.