ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mzinda uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao.
Masalimo 78:6 - Buku Lopatulika kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa, ngakhale ana amene sanabadwe, ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso. |
ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mzinda uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao.
Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.
Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.
Penyetsetsani malinga ake, yesetsani zinyumba zake; kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.
Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita mu Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.
Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.
Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu mu Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo padziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.