Masalimo 78:53 - Buku Lopatulika Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, kotero kuti sanaope; koma nyanja inamiza adani ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, kotero kuti sanaope; koma nyanja inamiza adani ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha koma nyanja inamiza adani awo. |
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.
Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.