Masalimo 78:51 - Buku Lopatulika Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu |
Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.
ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.
Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.