Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele.
Masalimo 78:41 - Buku Lopatulika Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kaŵirikaŵiri ankamuyesa, ankamputa Woyera wa Israele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu; ankamuputa Woyera wa Israeli. |
Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele.
Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;
amene makolo athu sanafune kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,