Masalimo 78:34 - Buku Lopatulika Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ankapha ena, otsalira ankayamba kumufunafuna. Ankalapa namafunafuna Mulungu ndi mtima wao wonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo; iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu. |
Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!
Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.
Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.
Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.
Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.