Masalimo 78:3 - Buku Lopatulika Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa, ndipo makolo athu anatifotokozera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa, ndipo makolo athu anatifotokozera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa zinthu zimene tidazimva ndi kuzidziŵa, zomwe makolo athu adatifotokozera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero zimene tinazimva ndi kuzidziwa, zimene makolo athu anatiwuza. |
Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.
Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mzinda wa Yehova wa makamu, m'mzinda wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.
ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita mu Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.
Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine mu Ejipito.
Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.