pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira, ndipo anapha mwa onenepa ao, nagwetsa osankhika a Israele.
Masalimo 78:21 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Yehova anamva, nakwiya; ndipo anayatsa moto pa Yakobo, ndiponso mkwiyo unakwera pa Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Yehova anamva, nakwiya; ndipo anayatsa moto pa Yakobo, ndiponso mkwiyo unakwera pa Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake Chauta atamva zimenezi, adapsa mtima kwambiri, adayatsira moto Yakobe, napambana kukwiyira Israeleyo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova atawamva anakwiya kwambiri; moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo, ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli, |
pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira, ndipo anapha mwa onenepa ao, nagwetsa osankhika a Israele.
Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.
Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.
Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.
Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.