Masalimo 78:16 - Buku Lopatulika Anatulukitsa mitsinje m'thanthwe, inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anatulukitsa mitsinje m'thanthwe, inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatumphutsa mifuleni m'thanthwe, nayendetsa madzi ngati mitsinje. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala ndi kuyenda madzi ngati mitsinje. |
amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.
Munapombosola uta wanu; malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona. Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.
Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.
amene anakutsogolerani m'chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;
Ndipo ndinatenga tchimo lanu, mwanawang'ombe mudampangayo, ndi mumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati fumbi; ndipo ndinataya fumbi lake m'mtsinje wotsika m'phirimo.