Ndipo anaiwala zochita Iye, ndi zodabwitsa zake zimene anawaonetsa.
Iwo adaiŵala zimene Mulungu adachita, ndiponso zozizwitsa zimene Iye adaŵaonetsa.
Anayiwala zimene Iye anachita, zozizwitsa zimene anawaonetsa.
Koma anaiwala ntchito zake msanga; sanalindire uphungu wake:
Ndi kuti chiyembekezo chao chikhale kwa Mulungu, osaiwala zochita Mulungu, koma kusunga malamulo ake ndiko.
Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.
Mwaleka Thanthwe limene linakubalani, mwaiwala Mulungu amene anakulengani.