si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.