Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Masalimo 78:1 - Buku Lopatulika Tamverani, anthu anga, chilamulo changa; tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tamverani, anthu anga, chilamulo changa; tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mvetsetsani zimene ndikukuphunzitsani, inu anthu anga. Tcherani khutu, mumve mau a pakamwa panga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa; mvetserani mawu a pakamwa panga. |
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena; Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe, Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.
Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.
Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu.
Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.
Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu; ndidzamuimbira ine Yehova, inetu; ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele.