Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.
Masalimo 77:4 - Buku Lopatulika Mundikhalitsa maso; ndigwidwa mtima wosanena kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundikhalitsa maso; ndigwidwa mtima wosanena kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumagwira zikope zanga kuti ndisagone tulo. Ndikuvutika kwambiri kotero kuti sindingathe kulankhula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munagwira zikope zanga kuti ndisagone ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule. |
Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.
Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukulu ndithu.
Pakuti zikadalemera tsopano koposa mchenga wa kunyanja; chifukwa chake mau anga ndasonthokera kunena.
Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.