Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.
Masalimo 77:3 - Buku Lopatulika Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika; ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika; ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikamalingalira za Mulungu, ndimangobuula mumtima. Ndikamasinkhasinkha za Iye, ndimataya mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula; ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka. Sela |
Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.
Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa, ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu.
Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
Potero sindidzaletsa pakamwa panga; ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga; ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.
Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda: Ndinamfunafuna, koma osampeza.