Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Masalimo 77:2 - Buku Lopatulika Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lamavuto ndimafunafuna Ambuye. Usiku wonse ndimakweza manja anga ndi kupemphera kosalekeza. Mtima wanga umakana kuusangalatsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye; usiku ndinatambasula manja mosalekeza ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa. |
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.
Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la mizinda yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse;
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.
Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.
Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.
Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.
Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.
Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Maria ananyamuka msanga, natuluka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,