A Yedutuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa chilangizo cha atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.
Masalimo 77:1 - Buku Lopatulika Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga; kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga; kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikulira mopemba kwa Mulungu, ndi mau okweza ndikufuula kwa Mulungu kuti andimve. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo; ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu. |
A Yedutuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa chilangizo cha atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.
Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.
Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.