Masalimo 76:9 - Buku Lopatulika pakuuka Mulungu kuti aweruze, kuti apulumutse ofatsa onse a padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuuka Mulungu kuti aweruze, kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pamene Inu Mulungu mudaimirira kuti muweruze anthu, ndi kupulumutsa opsinjidwa onse a pa dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze, kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko. Sela |
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.
Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.
Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo.
koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.