Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Masalimo 76:7 - Buku Lopatulika Inu ndinu woopsa; ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu ndinu woopsa; ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, Inu ndinu woopsa. Angathe kuima pamaso panu ndani pamene mkwiyo wanu wayaka? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa. Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya? |
Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m'kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.
Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.
Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.
Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.
Magaleta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m'nyanja; ndi akazembe ake osankhika anamira mu Nyanja Yofiira.
Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.
Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.
ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.