Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
Masalimo 76:3 - Buku Lopatulika Pomwepo anathyola mivi ya pauta; chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anathyola mivi ya pauta; chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumeneko adathyola mivi youluzika, zishango, malupanga ndi zida zonse zankhondo za adani ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka, zishango ndi malupanga, zida zankhondo. Sela |
Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.
Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m'matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo.
Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.