Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m'matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo.
pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.
Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.