Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Masalimo 76:1 - Buku Lopatulika Mulungu adziwika mwa Yuda, dzina lake limveka mwa Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu adziwika mwa Yuda, dzina lake limveka mwa Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu ndi wodziŵika m'dziko la Yuda, dzina lake ndi lolemekezeka mu Israele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu amadziwika mu Yuda; dzina lake ndi lotchuka mu Israeli. |
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.
Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.