Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete.
Masalimo 74:8 - Buku Lopatulika Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi; anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi; anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumtima mwao ankati, “Tiyeni tiŵagonjetse kotheratu.” Adatentha malo opatulika onse a Mulungu m'dzikomo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.” Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo. |
Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete.
Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete.
Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino.
Ndipo anaphunzitsa mu Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m'mizinda yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.
Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.
Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.