Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gadaa; munali mikungudza yokhayokha simunaoneke mwala ai.
Masalimo 74:6 - Buku Lopatulika Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zake zonse ndi nkhwangwa ndi nyundo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zake zonse ndi nkhwangwa ndi nyundo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake, ndi nsompho ndi nyundo, adakadzula zosemasema zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo zonse zimene tinapachika. |
Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gadaa; munali mikungudza yokhayokha simunaoneke mwala ai.
Nalemba m'makoma onse akuzinga chipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, m'katimo ndi kumbuyo kwake.
Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo wa azitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, nawakuta ndi golide; inde anakutanso ndi golide akerubi ndi migwalangwayo.
Ndipo analembapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, nakuta zolembazo ndi golide wopsapsala.