Tcherani khutu lanu, Yehova nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Senakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.
Masalimo 74:22 - Buku Lopatulika Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha; kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha; kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzambatukani, Inu Mulungu, tiyeni mudziteteze pa mlandu wanuwo, kumbukirani kuti anthu amwano amakunyodolani tsiku lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu; kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse. |
Tcherani khutu lanu, Yehova nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Senakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.
Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga, Mulungu wanga ndi Ambuye wanga.
Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.