Masalimo 74:16 - Buku Lopatulika Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu, munakonza kuunika ndi dzuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu, munakonza kuunika ndi dzuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudalenga usana ndi usiku. Mudaika mwezi ndi dzuŵa m'malo mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso; Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi. |
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.
Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;
kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.