Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 74:15 - Buku Lopatulika

Mudagawa kasupe ndi mtsinje; mudaphwetsa mitsinje yaikulu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mudagawa kasupe ndi mtsinje; mudaphwetsa mitsinje yaikulu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mudatumphutsa akasupe ndi mifuleni, mudaumitsa mitsinje imene siiphwa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje, munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.

Onani mutuwo



Masalimo 74:15
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.


Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.


Anatsegula pathanthwe, anatulukamo madzi; nayenda pouma ngati mtsinje.


Nyanjayo inaona, nithawa; Yordani anabwerera m'mbuyo.


Anang'alula thanthwe m'chipululu, ndipo anawamwetsa kochuluka monga m'madzi ozama.


Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m'dziko la Ejipito.


Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako;


Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.


Munapombosola uta wanu; malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona. Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.


Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe.


Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a mu Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka mu Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse.


Ndipo wachisanu ndi chimodzi anatsanulira mbale yake pamtsinje waukulu Yufurate; ndi madzi ake anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ochokera potuluka dzuwa.