Masalimo 74:14 - Buku Lopatulika Mudaphwanya mitu ya Leviyatani; mudampereka akhale chakudya cha zilombo za m'chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudaphwanya mitu ya Leviyatani; mudampereka akhale chakudya cha zilombo za m'chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudatswanya mitu ya Leviyatani, chilombo cham'madzi chija, nkuitaya kuti ikhale chakudya cha zilombo zam'chipululu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu. |
Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m'manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m'mphepete mwa nyanja.
Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.
Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.
Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi,