Masalimo 74:12 - Buku Lopatulika Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale, wochita zakupulumutsa pakati padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale, wochita zakupulumutsa pakati pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe Inu Mulungu, ndinu mfumu yanga kuyambira kalekale. Ndinu amene mumagwira ntchito yopulumutsa pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale; Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi. |
M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.
Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.
Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.
popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?