Masalimo 74:11 - Buku Lopatulika Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu? Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu? Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa chiyani mukubisa dzanja lanu lotithandiza? Bwanji dzanja lanu lamanja likungokhala pachifuwa panu? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja? Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge! |
Kodi mudzadziletsa pa zinthuzi, Yehova? Kodi Inu mudzakhala chete ndi kutivutitsa ife zolimba?
Pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Israele; wabweza m'mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo, natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.
Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.