Masalimo 74:10 - Buku Lopatulika Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, adani athuŵa adzanyodolabe mpaka liti? Amaliwongowo adzanyozabe dzina lanu mpaka muyaya? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu? Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya? |
Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.
Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.
Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?
Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele.
Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?
ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?