Masalimo 73:8 - Buku Lopatulika Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa, alankhula modzitama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa, alankhula modzitama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amanyodola ndi kumalankhula zoipa, amadzikuza ndi kumaopseza ena kuti, “Tikupsinjani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwowo amanyogodola ndi kumayankhula zoyipa; mwa kudzikuza kwawo amaopseza ena nʼkumati, “Tikuponderezani.” |
Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.
koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;
Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;
Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.
Ndipo m'dziko lonse la Israele simunapezeke wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisraele angadzisulire malupanga kapena mikondo;