Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake;
Masalimo 73:6 - Buku Lopatulika Chifukwa chake kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao; achivala chiwawa ngati malaya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao; achivala chiwawa ngati malaya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake amavala kunyada ngati mkanda wam'khosi. Amavala nkhanza ngati malaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake kunyada kuli monga mkanda wa mʼkhosi mwawo; amadziveka chiwawa. |
Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake;
Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye.
Anavalanso temberero ngati malaya, ndipo lidamlowa m'kati mwake ngati madzi, ndi ngati mafuta m'mafupa ake.
Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.
Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi; walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi, ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako.
Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.
Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.
Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m'manja mwako, ndi unyolo m'khosi mwako.
Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?
Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;
Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Ndipo kulemera kwake kwa maperere agolide adawapempha ndiko masekeli chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zovala zachibakuwa za pa mafumu a ku Midiyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamira zao.