Masalimo 73:22 - Buku Lopatulika ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndinali wopusa wosamvetsa kanthu, ndinali ngati chilombo kwa Inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndinali wopusa ndi wosadziwa; ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu. |
Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.
Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.
chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha.
Ndinati mumtima mwanga, kuti izi zichitika ndi ana a anthu, kuti Mulungu awayese ndi kuti akazindikire eni ake kuti ndiwo nyama zakuthengo.
Ng'ombe idziwa mwini wake, ndi bulu adziwa pomtsekereza: koma Israele sadziwa, anthu anga sazindikira.