kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
Masalimo 73:12 - Buku Lopatulika Tapenyani, oipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tapenyani, oipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onani, umu ndimo m'mene aliri anthu oipa. Nthaŵi zonse ali pabwino, ndipo amangolemera kosalekeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Umu ndi mmene oyipa alili; nthawi zonse ali pabwino ndipo chuma chawo chimachulukirachulukira. |
kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.
Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.
Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.
Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.
Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;