Masalimo 73:11 - Buku Lopatulika Namati, Akachidziwa bwanji Mulungu? Kodi Wam'mwambamwamba ali nayo nzeru? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Namati, Akachidziwa bwanji Mulungu? Kodi Wam'mwambamwamba ali nayo nzeru? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amati, “Kodi Mulungu angadziŵe bwanji? Kodi Wopambanazonseyo angadziŵe kanthu kalikonse?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amati, “Kodi Mulungu angadziwe bwanji? Kodi Wammwambamwamba angadziwe kalikonse?” |
Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.
Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.
Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.