Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:
Masalimo 72:9 - Buku Lopatulika Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amaliwongo akuchipululu adzaiŵeramira, adani ake adzadya fumbi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake ndipo adani ake adzanyambita fumbi. |
Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.
Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.