Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Masalimo 72:13 - Buku Lopatulika Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa. |
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.