Masalimo 71:6 - Buku Lopatulika Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu; Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga, ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse. |
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.
Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.
Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;
Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wake, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israele asonkhanidwe kwa Iye; chifukwa Ine ndili wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;
Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.
Kodi kuyambira tsopano sudzafuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?
Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,
ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;