Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.
Masalimo 71:18 - Buku Lopatulika Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu musanditaye Inu Mulungu, mpaka nditalengeza mphamvu zanu kwa mibado yonse yakutsogolo. |
Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.
Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.
Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.
Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.
kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao.
Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine mu Ejipito.
ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.
Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?
Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;
Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.
Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai.