Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Masalimo 71:15 - Buku Lopatulika Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakamwa panga padzalankhula tsiku lonse za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu, popeza kuti sindidziŵa chiŵerengero chake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu, za chipulumutso chanu tsiku lonse, ngakhale sindikudziwa muyeso wake. |
Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.
Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.
Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.
Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.
Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.