Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.
Masalimo 71:14 - Buku Lopatulika Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ine ndidzakhulupirira Inu nthaŵi zonse, ndipo ndidzapitirizabe kukutamandani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse, ndidzakutamandani mowirikizawirikiza. |
Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.
Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse;
pakutinso munawachitira ichi abale onse a mu Masedoniya yense. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa,
Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu;
Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.
Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.