Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 71:13 - Buku Lopatulika

Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu ondineneza achite manyazi ndipo aonongeke. Anthu ofunafuna kundipweteka anyozedwe, ndipo achite manyazi kotheratu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi, iwo amene akufuna kundipweteka avale chitonzo ndi manyazi.

Onani mutuwo



Masalimo 71:13
12 Mawu Ofanana  

pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'mizinda mwao, m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, kuwathira manja ofuna kuwachitira choipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.


Otsutsana nane avale manyazi, nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda.


Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.


Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.


Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.


Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu adani anga onse; adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.


Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao amene akuti, Hede, hede.


Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.


Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati chabe, nadzaonongeka.


Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.


Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.