Masalimo 71:11 - Buku Lopatulika ndi kuti, Wamsiya Mulungu. Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi kuti, Wamsiya Mulungu. Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa namanena kuti, “Mulungu wamsiya yekha. Mlondoleni, mumgwire, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe woti ampulumutse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amati, “Mulungu wamusiya; mutsatireni ndi kumugwira, pakuti palibe amene adzamupulumutse.” |
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.
Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?
Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.