Masalimo 7:15 - Buku Lopatulika Anachita dzenje, nalikumba, nagwa m'mbuna yomwe anaikumba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anachita dzenje, nalikumba, nagwa m'mbuna yomwe anaikumba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amakumba mbuna kuti ikhale yozama, koma amagwamo ndiye yemwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa amagwera mʼdzenje limene wakumbalo. |
Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.
Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumalizani inu.
Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.
Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.
Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu.