Masalimo 7:14 - Buku Lopatulika Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake; anaima ndi chovuta, nabala bodza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake; anaima ndi chovuta, nabala bodza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, munthu woipa amalingalira zoipa zokhazokha nthaŵi zonse, ntchito yake ndi kunyenga ndi kuvutitsa anthu ena basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse. Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena. |
Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumalizani inu.
Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.