Masalimo 69:36 - Buku Lopatulika Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira; ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m'mwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira; ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m'mwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a atumiki ake nawonso adzalilandira kuti likhale lao, ndipo okonda Mulungu adzakhala m'menemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo, ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko. |
Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.
Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?
ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.