Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.
Masalimo 69:32 - Buku Lopatulika Ofatsa anachiona, nakondwera, ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ofatsa anachiona, nakondwera, ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ozunzika aone zimenezo ndipo asangalale, inu amene mumafunafuna Mulungu, mulimbenso mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wosauka adzaona ndipo adzasangalala, Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo! |
Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.
Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.
Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.
Ndipo pamene adanena ichi, anaonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera pakuona Ambuye.