Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Masalimo 69:31 - Buku Lopatulika Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng'ombe, inde mphongo za nyanga ndi ziboda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng'ombe, inde mphongo za nyanga ndi ziboda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimenezi zidzakondwetsa Chauta kupambana nsembe, ngakhale nsembe ya ng'ombe yamphongo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe, kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake. |
Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.